Kodi Cipembedzo Mungacikhulupilile Pankhani ya Nkhondo?
Alberto anagwila nchito yausilikali zaka pafupi-fupi 10. Iye anati: “Mtsogoleli wathu wa cipembedzo anali kutidalitsa akumati, ‘Mulungu ali ndi inu.’ Koma ndinali kudzifunsa kuti, ‘Ndikupita kukapha anthu, pamene Baibo imanena kuti “usaphe.”’”
Ray anali m’gulu la asilikali apamadzi panthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Nthawi ina anafunsa mtsogoleli wao wa cipembedzo kuti: “Mumaloŵa mu combo ndi kutipemphelela kuti tikapambane. Kodi adani athu naonso sacita cimodzi-modzi?” Mtsogoleli wa cipembedzo anayankha kuti Ambuye amacita zinthu m’njila zodabwitsa.
Ngati yankho limenelo lakudabwitsani, dziŵani kuti simuli nokha.
ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA
Yesu ananena kuti limodzi mwa malamulo aakulu a Mulungu ndi lakuti, “uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Maliko 12:31) Kodi Yesu anati tiyenela kukonda anzathu cifukwa ca kumene io amakhala kapena cifukwa ca mtundu wao? Iyai. Iye anauza ophunzila ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Iwo anafunika kukondana kwambili cakuti cikondico cinayenela kukhala cizindikilo cao. Ndipo anali okonzeka kufela anzao, m’malo mowapha.
Akristu oyambilila anali kutsatila mau a Yesu. Buku lina linati: “Abambo a chalichi coyambilila, kuphatikizapo Tertullian ndi Origen, anavomeleza kuti Akristu analetsedwa kupha munthu, ndipo lamulo limeneli linawaletsa kutenga mbali m’gulu la nkhondo la Roma.”—The Encyclopedia of Religion.
KODI MBONI ZA YEHOVA ZIMACITA BWANJI PANKHANIYI?
Mboni za Yehova zimapezeka pafupi-fupi m’maiko onse, ndipo nthawi zina ena amakhala m’maiko amene ali pa udani ndi dziko lina. Koma io amayesetsa kuonetsa cikondi cimene ndi cizindikilo ca Akristu oona.
Mwacitsanzo, pamene mitundu ya Ahutu ndi Atutsi inali kulimbana ku Rwanda mu 1994, Mboni za Yehova sizinatengeko mbali ngakhale pang’ono pa nkhondo imeneyo. Mboni za Cihutu ndi Citutsi zinali kubisana, ngakhale kuti kucita zimenezo kunaika miyoyo yao pangozi. Pamene Mboni ziŵili za Cihutu zinagwidwa cifukwa cobisa abale ao a Citutsi, gulu la Interahamwe la Cihutu, linati: “Mudzaphedwa cifukwa munathandizila Atutsi kuthaŵa.” Ndipo, n’zomvetsa cisoni kuti pambuyo pake Mboni ziŵili za Cihutu zija zinaphedwa.—Yohane 15:13.
Muganiza bwanji: Kodi zocita za Mboni za Yehova ndi zogwilizana ndi mau a Yesu pankhani yoonetsa cikondi codzimana?
[Eni ake]
Based on U.S. Army photo
[Mau okopa papeji 5]
Kodi atsogoleli a cipembedzo amaphunzitsa anthu kukhala ndi cikondi ceni-ceni cacikristu?