Kodi Pali Cipembedzo Cimene Mungakhulupilile?
Ngati munakhumudwa cifukwa ca cipembedzo cinacake, zingakhale zovuta kuti mukhulupilile cipembedzo ciliconse. Koma dziŵani kuti cipembedzo cimene mungakhulupilile cilipo. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anasonkhanitsa gulu la otsatila ake okhulupilika ndipo anawaphunzitsa kutsatila mfundo za Mulungu pa umoyo wao. Otsatila oona a Kristu, kutanthauza anthu amene amayesetsa kutsatila mfundo za Cikristu pa umoyo wao, alipo. Kodi anthu amenewa mungawapeze kuti?
Estelle, amene tam’chula m’nkhani yaciŵili, anati: Ndinayamba kudziŵa Baibo pamene ndinayamba kuphunzila ndi Mboni za Yehova. Sipanapite nthawi yaitali kuti ndimvetsetse zimene lemba la Yohane 8:32 limanena. Lembalo limati: “Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.’”
Ray, amenenso tam’chula kale, anati: “Cifukwa cophunzila Baibo ndi Mboni za Yehova, ndinadziŵa kuti si Mulungu amene amacititsa mavuto amene ife anthu timakumana nao. Ndinasangalala kudziŵa kuti ngakhale kuti Mulungu ali ndi zifukwa zabwino zololela zinthu zoipa pakali pano, iye watilonjezanso kuti adzacotsapo mavuto amenewa posacedwapa.”
Mosakaikila, n’kovuta kucita zinthu zabwino pamene anthu ambili ali ndi makhalidwe oipa. Koma zimenezi n’zotheka. Anthu ambili amafuna thandizo kuti amvetsetse Baibo ndi kugwilitsila nchito zimene imanena. N’cifukwa cake Mboni za Yehova zimacititsa maphunzilo a Baibo a panyumba kwaulele kwa anthu mamiliyoni ambili padziko lonse lapansi. Mlungu uliwonse, anthu ambili-mbili akuphunzila zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni. Ndipo cotulukapo n’cakuti anthu amenewo akuyandikila kwa Mlengi wao, ndipo ndi osangalala pa umoyo wao.a
Pamene mudzakumana ndi Mboni za Yehova, bwanji osazifunsa cifukwa cake zimakhulupilila cipembedzo cao? Fufuzani ziphunzitso zao ndi mbili yao. Ndiyeno muone ngati pali cipembedzo cimene mungakhulupilile.
[Mau apansi]
a Kuti mumve zambili onani buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mau okopa papeji 7]
Bwanji osafunsa Mboni za Yehova cifukwa cake zimakhulupilila cipembedzo cao?