Kodi Tinacokela Kuti?
Buku loyamba m’Baibo limene ndi Genesis, limafotokoza mwacidule ciyambi ca cilengedwe conse kuti: “Paciyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Pambuyo polenga zomela ndi nyama, Mulungu analenga anthu oyambilila, Adamu ndi Hava. Iwo anali osiyana ndi nyama cifukwa cakuti anali ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu, kuphatikizapo ufulu wodzisankhila zocita. Conco, zosankha zao zikanapangitsa kuti aimbidwe mlandu kapena kudalitsidwa. Iwo akanamvela malangizo a Mulungu, akanakhala makolo a anthu onse amene anayenela kusangalala ndi mtendele ndiponso moyo wangwilo padziko lapansi kwamuyaya mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.
Komabe, mngelo wina kapena kuti colengedwa cauzimu, anagwilitsila nchito anthu kuti akwanilitse zofuna zake zadyela. Conco, iye anakhala Satana kutanthauza “Wotsutsa.” Mwa kugwilitsila nchito njoka, Satana ananamiza Hava kuti angakhale ndi moyo wabwino popanda kudalila Mulungu. Adamu ndi Hava anamvela Satana, ndipo anaononga ubwenzi wao ndi Mlengi wao. Cifukwa cosankha molakwika, makolo athu oyambilila anataya mwai wokhala ndi moyo wamuyaya, ndipo anapatsila ife tonse ucimo, kupanda ungwilo ndi imfa.
Mwamsanga, Mulungu analengeza cifunilo cake cothetsa mavuto amenewa kuti apeleke kwa mbadwa za Adamu mwai wokhala ndi moyo wamuyaya. Mulungu ananenelatu kuti “mbeu,” kutanthauza munthu wina wapadela, adzaononga Satana ndi kucotsapo mavuto onse amene Satana, Adamu ndi Hava anabweletsa. (Genesis 3:15) Kodi ndani amene anali kudzakhala “mbeu” imeneyo? Zimenezi zinadziŵika patapita nthawi.
Komabe, Satana nthawi zonse anali kuyesa-yesa kulepheletsa cifunilo cabwino ca Mulungu. Ucimo ndi kuipa zinafalikila kwambili. Mulungu anaganiza zoononga anthu oipa ndi cigumula. Iye analamula Nowa munthu wolungama kumanga cingalawa cacikulu, kuti iye ndi banja lake akapulumuke pamodzi ndi nyama zimene anauzidwa kuloŵetsa m’cingalawa.
Pambuyo pa caka cimodzi Cigumula citayamba, Nowa ndi banja lake anatuluka m’cingalawa ndi kukhala pa dziko loyeletsedwa. Koma “mbeu” imeneyo inali isanadziŵike.
—Yazikidwa pa Genesis caputala 1 mpaka 11; Yuda 6, 14, 15; Chivumbulutso 12:9.