LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsa. 5
  • Mulungu Anakonza Njila Yopulumutsila Anthu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Anakonza Njila Yopulumutsila Anthu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 10/1 tsa. 5

Mulungu Anakonza Njila Yopulumutsila Anthu

Mulungu analonjeza Abulahamu kuti “mbeu” yolonjezedwa idzakhala mbadwa yake. Kupyolela mwa munthu ameneyo, anthu a “mitundu yonse” adzadalitsidwa. (Genesis 22:18) Nthawi ina, Yakobo mdzukulu wa Abulahamu anapita ku Iguputo, ndipo kumeneko banja lake linakhala mtundu wa Isiraeli.

Patapita nthawi, Farao mfumu yankhanza ya Iguputo inayamba kuvutitsa Aisiraeli. Conco, Mulungu anatumiza mneneli Mose kuti atsogolele Aisiraeli kucoka m’dziko limenelo mwa kuoloka Nyanja Yofiila mozizwitsa. Pambuyo pake, Mulungu anapatsa Aisiraeli Malamulo Khumi ndi malamulo ena kuti aziwatsogolela ndi kuwateteza. Malamulo amenewo anali okhudza kupeleka nsembe kuti macimo ao akhululukidwe. Mouzilidwa ndi Mulungu, Mose anauza Aisiraeli kuti Mulungu adzatumiza mneneli wina. Mneneli ameneyo ndiye anali “mbeu” yolonjezedwa.

Pambuyo pa zaka zoposa 400, Mulungu analonjeza Mfumu Davide kuti “mbeu” imene inalonjezedwa mu Edeni, idzalamulila mu ufumu umene sudzatha. Mbeu imeneyo ndi Mesiya, Mpulumutsi woikidwa ndi Mulungu kuti apulumutse anthu ndi kubwezeletsa Paladaiso padziko lapansi.

Kupyolela mwa Davide ndi aneneli ena, Mulungu pang’ono-pang’ono anavumbula zinthu zina ponena za Mesiya. Iwo ananena kuti Mesiya adzakhala wodzicepetsa ndi wokoma mtima, ndi kuti mu ulamulilo wake simudzakhala njala, kusalungama ndi nkhondo. Anthu onse adzakhala pa mtendele ndi anthu anzao ndiponso ndi nyama. Matenda, kuvutika ndi imfa sizinali mbali ya cifunilo coyambilila ca Mulungu. Conco, Mulungu adzathetsa zimenezi ndipo anthu amene anamwalila adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.

Kupyolela mwa mneneli Mika, Mulungu anakamba kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu, ndipo kupyolela mwa mneneli Danieli anakamba kuti Mesiya adzaphedwa. Koma Mulungu anali kudzaukitsa Mesiya ndi kumuika kukhala Mfumu kumwamba. Komanso Danieli anaona m’masomphenya kuti pambuyo pake Ufumu wa Mesiya udzaononga maufumu onse ndi kulamulila kwamuyaya. Kodi Mesiya anabweladi mogwilizana ndi ulosi?

—Yazikidwa pa Genesis caputala 22 mpaka 50 ndiponso Ekisodo, Deuteronomo, 2 Samueli, Masalimo, Yesaya, Danieli, Mika, Zekariya 9:9.

[Caption on page 5]

DZINA LOYELA LA MULUNGU

Dzina lakuti Yehova limapezeka koyamba m‘Baibo pa lemba la Genesis 2:4. Dzina lapadela limeneli limapezeka nthawi pafupi-fupi 7,000 mu mipukutu ya cinenelo coyambilila ca Malemba Opatulika. Tanthauzo lake lakuti “Amacititsa kukhala,” limatitsimikizila kuti Mulungu sangalephele kukwanilitsa cifunilo cake ndi malonjezo ake onse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani