NKHANI YA PACIKUTO | MABODZA AMENE AMALEPHELETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU
Bodza Lakuti Mulungu Alibe Dzina
ZIMENE ANTHU AMBILI AMAKHULUPILILA “Sitinagwilizane kuti kaya Mulungu ali ndi dzina kapena ai. Ndipo ngati ali nalo, sitinagwilizanenso kuti iye ndani.”—Pulofesa David Cunningham, Theological Studies.
ZIMENE BAIBO IMANENA Mulungu anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) “Yehova” ndi dzina la Ciheberi limene limatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.”—Onani Baibulo la Dziko Latsopano, Zakumapeto 1, ndime 1.
Yehova amafuna kuti tizigwilitsila nchito dzina lake. Baibo imati: “Itanani pa dzina lake. Dziŵitsani mitundu ya anthu zocita zake. Nenani kuti dzina lake n’lokwezeka.”—Yesaya 12:4.
Yesu anali kugwilitsila nchito dzina la Mulungu. M’pemphelo lake, iye anauza Yehova kuti: “Ine ndacititsa kuti io [ophunzila a Yesu] adziŵe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziŵitsa dzinalo.” N’cifukwa ciani Yesu anadziŵitsa ophunzila ake dzina la Mulungu? Iye anati: “Kuti cikondi cimene munandikonda naco cikhale mwa io, inenso ndikhale wogwilizana ndi io.”—Yohane 17:26.
N’CIFUKWA CIANI KUDZIŴA ZIMENEZI N’KOFUNIKA? Katswili wa maphunzilo a zaumulungu wochedwa Walter Lowrie, analemba kuti: “Munthu amene sadziŵa dzina la Mulungu ndiye kuti samudziŵadi Mulungu, ndipo munthuyo sangathe kukonda Mulungu.”
Ngakhale kuti mwamuna wina wochedwa Victor anali kupita kuchechi mlungu uliwonse, iye anali kuonabe kuti sadziŵa Mulungu. Victor anati: “Ndiyeno ndinaphunzila kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndipo zinali ngati kuti iye akudzidziŵikitsa kwa ine. Ndinaona ngati ndakumana ndi Munthu amene ndakhala ndikumva mbili yake kwa nthawi yaitali. Ndinamudziŵa bwino, ndipo ndinakhala naye pa ubwenzi.”
Yehova amayandikila anthu amene amagwilitsila nchito dzina lake. Ponena za “anthu amene anali kuganizila za dzina lake,” Mulungu analonjeza kuti: “Ndidzawacitila cifundo monga mmene munthu amacitila cifundo mwana wake amene amamutumikila.” (Malaki 3:16, 17) Ndipo Mulungu amadalitsanso anthu amene amaitana pa dzina lake. Baibo imati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.