NKHANI YA PACIKUTO | MABODZA AMENE AMALEPHELETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU
Coonadi Cingakumasuleni
Tsiku lina ku Yerusalemu, Yesu anali kuphunzitsa za Atate wake, Yehova, ndi kuvumbula cinyengo ca atsogoleli onama a cipembedzo. (Yohane 8:12-30) Zimene Yesu anakamba panthawiyo zimatithandiza kufufuza zimene timakhulupilila ponena za Mulungu. Yesu anati: “Mukamasunga mau anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.”—Yohane 8:31, 32.
Mau aYesu akuti “mukamasunga mau anga nthawi zonse,” akusonyeza kuti kudziŵa mau ake kungatithandize kupenda ziphunzitso za cipembedzo kuti tione ngati ndi “coonadi”. Mukamva mfundo ina yake yonena za Mulungu, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zikugwilizana ndi mau a Yesu ndiponso zimene Malemba onse amanena?’ Tengelani citsanzo ca anthu amene anamva mau a Paulo. Iwo “anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizile ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.”—Machitidwe 17:11.
Marco, Rosa, ndi Raymonde, amene tawachula m’nkhani yoyamba ija, anafufuza mosamala zimene anali kukhulupilila. Iwo anacita zimenezi mwa kuphunzila Baibo ndi Mboni za Yehova. Kodi anapindula bwanji ndi zimene anaphunzila?
Marco: “Munthu amene anali kutiphunzitsa Baibo anagwilitsila nchito Malemba kuyankha mafunso onse amene ine ndi mkazi wanga tinali nao. Tinayamba kukonda kwambili Yehova ndipo ine ndi mkazi wanga tinayamba kukondana kwambili.”
Rosa: “Poyamba, ndinali kuganiza kuti Baibo ndi buku la nzelu za anthu limene limafotokoza za Mulungu. Koma pambuyo pophunzila Baibo ndinapeza mayankho a mafunso anga onse. Tsopano Yehova ndi weni-weni kwa ine, ndipo ndimamudalila.”
Raymonde: “Ndinali kupemphela kwa Mulungu kuti andithandize kumudziŵa bwino. Patapita nthawi yocepa, ine ndi mwamuna wanga tinayamba kuphunzila Baibo. Tinadziŵa coonadi ponena za Yehova. Tinasangalala kwambili pamene tinadziŵa mmene Mulungu alili.”
Baibo imavumbula mabodza onena za Mulungu komanso imatithandiza kudziŵa makhalidwe ake abwino. Iyo ndi Mau ake ouzilidwa, ndipo imatithandiza ‘kudziŵa zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.’ (1 Akorinto 2:12) Kodi mungakonde kudziŵa mayankho a m’Baibo pa mafunso ofunika kwambili okhudza Mulungu, colinga cake ndi tsogolo lathu? Ngati ndi conco, ŵelengani mayankho a mafunso ena a m’Baibo pa Webusaiti ya www.jw.org pa mutu wakuti “Ziphunzitso za m’Baibo > Kuyankha Mafunso a m’Baibo.” Mungapemphenso phunzilo la Baibo pa Webusaiti imeneyi kapena kwa mmodzi wa Mboni za Yehova. Tikhulupilila kuti mukacita zimenezi, mudzaona kuti Mulungu ndi wabwino ndipo mudzamukonda.