LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 1 masa. 10-13
  • ‘Mulungu Anakondwela Naye’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Mulungu Anakondwela Naye’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “INOKI ANAYENDABE NDI MULUNGU WOONA”
  • “INOKI ANALOSELA ZA IWOWA”
  • “ANASAMUTSIDWA KUTI ASAFE MOZUNZIKA”
  • Munthu Wopanda Mantha
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 1 masa. 10-13
Inoki

TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO INOKI

‘Mulungu Anakondwela Naye’

INOKI anakhala na moyo kwa zaka zambili. N’zocititsa cidwi kuti Inoki anakhala na moyo zaka 365. Zaka zimenezi n’zoculuka kuposa zaka za anthu anayi okalamba ngako masiku ano. Ngakhale kuti anali na zaka zambili conco, iye sanali okalamba kweni-kweni. Nthawi imeneyo, zaka zoposa 5,000 zapita, anthu anali kukhala na moyo zaka zambili kuposa masiku ano. Mwacitsanzo, Adamu anali na zaka zoposa 600 pamene Inoki anabadwa. Ndipo iye anakhalabe na moyo zaka zina 300. Mbadwa zina za Adamu zinakhala na moyo kuposa pamenepo. Conco, ngakhale kuti Inoki anali na zaka 365, anali kuonekabe wamphamvu cakuti akanapitiliza kukhala na moyo kwa zaka zina zambili. Koma sizinatheke.

Moyo wa Inoki unali pangozi. Yelekezelani kuti mukumuona akuthawa kuti abisale kwa adani ake. Akucita mantha ndi anthu amene akwiya cifukwa cowauza uthenga wocokela kwa Mulungu. Nkhope zawo zinali na makwizi cifukwa ca ukali. Anthu amenewo anali kumuzonda ngako. Anali kuzondanso uthenga wake ndi Mulungu amene anam’tuma. Koma popeza kuti sakanatha kulimbana ndi Yehova, Mulungu wa Inoki, iwo anafuna kupha Inokiyo. N’kutheka kuti Inoki anayamba kuganiza kuti sadzaonananso ndi a m’banja lake. Mwina iye anali kuganizila za mkazi wake, ana ake aakazi, mwana wake wamwamuna Metusela, kapena mdzukulu wake Lameki. (Genesis 5:21-23, 25) Kodi awa ndiwo anali mapeto a moyo wake?

Inoki sachulidwa kaŵili-kaŵili m’Baibo. Pali Malemba atatu cabe amene amakamba za Inoki. (Genesis 5:21-24; Aheberi 11:5; Yuda 14, 15) Ngakhale n’conco, mavesi ocepa amenewo amatipatsa cithunzi cokwanila cakuti Inoki anali munthu wa cikhulupililo colimba. Kodi mumasamalila banja? Kodi anthu ena anakuvutitsamponi cifukwa cocita zinthu zabwino molimba mtima? Ngati n’conco, ndiye kuti muphunzila zambili pa cikhulupililo cimene Inoki anali naco.

“INOKI ANAYENDABE NDI MULUNGU WOONA”

Pa nthawi imene Inoki anabadwa, anthu anali kucita zoipa. Inoki anali wa mu m’badwo wa 7 kucokela kwa Adamu. Panthawiyo, anthu anali pafupi kwambili na ungwilo umene Adamu na Hava anataya. Ndiye cifukwa cake anthu anali kukhala na moyo zaka zambili. Ngakhale zinali conco, iwo anali na makhalidwe oipa ndipo sanali paubwenzi wabwino na Mulungu. Ciwawa cinali ponse-ponse. Khalidwe limeneli linayambila mu m’badwo waciŵili, pamene Kaini anapha m’bale wake Abele. Ndipo m’modzi wa mbadwa za Kaini anali wankhanza kwambili ndi wokonda kubwezela kuposa Kainiyo, cakuti anali kucita kunyadila. Komanso pofika mu m’badwo wacitatu, anthu anayamba kucita zinthu zoipa ngako. Anayamba kuitanila pa dzina la Yehova, koma osati monga olambila oona a Mulungu. Mwacionekele, anali kuchula dzina la Mulungu monyoza ndi mopanda ulemu.—Genesis 4:8, 23-26.

Kulambila konama kumeneku kunali kofala m’nthawi ya Inoki. Conco, pamene iye anali kukula, anafunika kupanga cosankha. Anafunika kusankha kaya kutengela zocita za anthu a m’nthawi yake, kapena kufuna-funa Yehova, Mulungu woona, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. Inoki ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili ataphunzila za Abele, amene anaphedwa cifukwa colambila Yehova m’njila yoyenela. Inoki anasankha kutengela cikhulupililo ca Abele. Pa Genesis 5:22 pamati: “Inoki anayendabe ndi Mulungu woona.” Mau amenewa aonetsa kuti Inoki anali kuopa Mulungu ngakhale kuti anali kukhala ndi anthu osaopa Mulungu. Iye ndi munthu woyamba kuchulidwa m’Baibo kuti anayendabe ndi Mulungu.

Vesi imodzimodziyo ikamba kuti Inoki anapitiliza kuyenda na Yehova pambuyo pobeleka Metusela. Conco, tingathe kuona kuti Inoki anakhala na banja ali na zaka pafupi-fupi 65. Iye anali na mkazi, koma Baibo siichula dzina la mkaziyo. Analinso ndi “ana aamuna ndi aakazi,” koma ciŵelengelo cawo sicidziŵika. Kuti tate amene alela ana ndi kusamalila banja ayende na Mulungu, afunika kusamalilanso banjalo pa zinthu zauzimu. Inoki anadziŵa kuti Yehova afuna kuti iye akhale wokhulupilika kwa mkazi wake. (Genesis 2:24) Ndipo n’zosakayikitsa kuti anayesetsa kuphunzitsa ana ake za Yehova Mulungu. Kodi zotsatilapo zake zinali zabwanji?

Baibo siikamba zambili pa nkhani imeneyi. Siikamba ciliconse za cikhulupililo ca mwana wa Inoki, Metusela, amene anakhala na moyo wautali pa anthu onse ochulidwa m’Baibo. Metusela anakhala na moyo mpaka m’caka cimene kunacitika cigumula. Komabe, Metusela anabeleka mwana dzina lake Lameki. Lamekiyo atabadwa, Inoki, amene anali ambuye ake, anaptilizabe kukhala na moyo kwa zaka zoposa 100. Ndipo Lameki anakhala munthu wacikhulupililo colimba. Yehova anauzila Lamekiyo kukamba ulosi wokhudza mwana wake Nowa, ndipo ulosi umenewo unakwanilitsika pambuyo pa cigumula. Nowa anayenda ndi Mulungu mofanana ndi Inoki, ambuye wawo wa atate ŵake. Koma Nowa sanaonanepo ndi Inoki. Ngakhale n’conco, Inoki anasiyila Nowa citsanzo cabwino. Nowa ayenela kuti anaphunzila za cikhulupililo ca Inoki, kucokela kwa Lameki, atate ŵake, kapena kucokela kwa Metusela, ambuye ake. N’kuthekanso kuti anaphunzila zimenezi kwa Yaredi, atate a Inoki, amene anamwalila pamene Nowa anali na zaka 366.—Genesis 5:25-29; 6:9; 9:1.

Ganizilani kusiyana pakati pa Adamu ndi Inoki. Ngakhale kuti Adamu anali wangwilo, anacimwila Yehova ndipo anasiyila ana ake mavuto na citsanzo coipa ca kupanduka. Koma Inoki, ngakhale kuti anali wopanda ungwilo, anayenda ndi Mulungu ndipo anasiyila mbadwa zake citsanzo cabwino ca cikhulupililo. Adamu anafa pamene Inoki anali na zaka 308. Kodi banja lake linalila malilo a kholo lodzikonda limeneli? Sitidziŵa. Koma cimene tidziŵa n’cakuti, Inoki, “anayendabe ndi Mulungu woona.”—Genesis 5:24.

Chati coonetsa anthu ochulidwa m’Baibo amene miyoyo yawo inapezana na moyo wa Inoki

Ngati musamalila banja, n’ciani cimene mungaphunzile pa cikhulupililo cimene Inoki anali naco? Kusamalila banja lanu pa zinthu zakuthupi n’kofunika. Koma cofunika ngako ndi kusamalila banja lanu pa zinthu zauzimu. (1 Timoteyo 5:8) Mungacite zimenezi osati mwa zokamba zanu cabe, komanso mwa zocita zanu. Mukasankha kuyenda na Mulungu mmene Inoki anacitila, na kulola Mau ouzilidwa a Mulungu kukutsogolelani pa umoyo wanu, mudzasiyila banja lanu citsanzo cabwino cofunika kutengela.

“INOKI ANALOSELA ZA IWOWA”

Monga munthu wa cikhulupililo, Inoki ayenela kuti anaona kuti ali yekha-yekha m’dziko la anthu osowa cikhulupililo. Koma kodi Mulungu wake, Yehova, anadziŵa mmene iye anali kumvelela? Inde. Tsiku lina, Yehova anakamba ndi mtumiki wake wokhulupilika ameneyo. Anamuuza uthenga wakuti alengeze kwa anthu a m’nthawi yake. Conco, Inoki anakhala mneneli woyamba amene uthenga wake unalembedwa m’Baibo. Tidziŵa zimenezi cifukwa Yuda, amene anali m’bale wake wa Yesu, anauzilidwa kulemba ulosi wa Inoki zaka zambili pambuyo pake.a

Kodi ulosi wa Inoki unali wabwanji? Unali wakuti: “Taonani! Yehova anabwela ndi miyandamiyanda ya oyela ake, kudzapeleka ciweluzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu cifukwa ca nchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazicita mosaopa Mulungu, komanso cifukwa ca zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ocimwa osaopa Mulungu anamunenela.” (Yuda 14, 15) Mwina mungadabwe kuti mu ulosi umenewu, Inoki anakamba monga kuti Mulungu anali atacita kale zimene ulosiwu unakamba. Umu ndi mmene maulosi ambili analembedwela pambuyo pake. Inoki anakamba ulosi umenewu monga kuti wacitika kale cifukwa zimene anali kukamba zinali zakuti zidzacitikadi zivute zitani.—Yesaya 46:10

Inoki alalikila anthu osaopa Mulungu

Inoki analengeza uthenga wa Mulungu molimba mtima kwa anthu aciwawa

Sicinali copepuka kuti Inoki alengeze uthenga waciweluzo umenewo kwa anthu onse amene anafunika kuumva. Onani kuti uthengawo unali wamphamvu kwambili. Mau akuti “anthu osaopa Mulungu,” anachulidwa kanayi pofuna kudzudzula anthu ndi nchito zawo zoipa. Conco, ulosiwo unali cenjezo kwa anthu onse. Unaonetsa kuti khalidwe lawo linafika poipa kwambili kucokela pamene anthu oyambilila anacotsedwa m’munda wa Edeni. Ulosi umenewo unaonetsanso kuti anthu a m’nthawi imeneyo adzawonongedwa pamene Yehova adzabwela ndi “miyandamiyanda ya oyela ake.” Oyela amenewa ndi magulu a angelo okonzeka kumenya nkhondo kuti awononge anthu oipa. Molimba mtima, Inoki analengeza uthenga wocenjeza umenewu wocokela kwa Mulungu ali yekha-yekha. Pa nthawiyi Lameki anali wamng’ono, ndipo n’kutheka kuti anacita cidwi ndi kulimba mtima kwa Inoki, ambuye ake. Ngati zinali conco, tingamvetsetse cifukwa cake.

Cikhulupililo ca Inoki ciyenela kutilimbikitsa kudzifufuza kuti tione ngati timaona dzikoli monga mmene Mulungu amalionela. Uthenga waciweluzo umene Inoki analengeza ni cenjezo kwa anthu onse masiku ano monga mmene zinalili m’nthawi ya Inoki. Mogwilizana ndi cenjezo la Inoki, Yehova anabweletsa cigumula camadzi cimene cinawononga anthu osaopa Mulungu m’masiku a Nowa. Koma zimene zinacitikazo ni citsanzo ca ciwonongeko cacikulu cimene cidzabwela mtsogolo. (Mateyu 24:38, 39; 2 Petulo 2:4-6) Molingana ndi masiku akale, masiku ano, Mulungu pamodzi ndi a angelo ake oyela ambili-mbili, ni okonzeka kupeleka ciweluzo kwa anthu osaopa Mulungu. Aliyense wa ife ayenela kumvela cenjezo la Inoki na kucenjezako ena. Tikacita zimenezo, acibale athu angaleke kugwilizana nafe ndipo tingayambe kuona kuti tilibe anzathu. Koma kumbukilani kuti Yehova sanamusiye Inoki, ndipo sangasiyenso atumiki ake okhulupilika masiku ano.

“ANASAMUTSIDWA KUTI ASAFE MOZUNZIKA”

Kodi Inoki anafa bwanji? Tingakambe kuti imfa yake inali yodabwitsa kwambili komanso yocititsa cidwi kuposa umoyo wake. Buku la Genesis limakamba cabe kuti: “Inoki anayendabe ndi Mulungu woona. Kenako iye sanaonekenso, cifukwa Mulungu anam’tenga.” (Genesis 5:24) Kodi Mulungu anatenga Inoki m’njila yabwanji? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mwa cikhulupililo, Inoki anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kwina kulikonse cifukwa Mulungu anamusamutsa. Pakuti asanasamutsidwe, Mulungu anamucitila umboni kuti akukondwela naye.” (Aheberi 11:5) Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti Inoki “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Mabaibo ena amakamba kuti Mulungu anatenga Inoki kupita naye kumwamba. Koma zimenezo si zoona. Takamba conco cifukwa Baibo imaonetsa kuti Yesu Khiristu ndiye anali woyamba kuukitsidwa kuti akakhale kumwamba.—Yohane 3:13.

Nanga Baibo itanthauza ciani pamene ikamba kuti Inoki “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Yehova ayenela kuti anacotsa moyo wa Inoki pang’no-pang’ono kuti asaphedwe mwankhanza ndi adani ake. Koma izi zikalibe kucitika, “Mulungu anamucitila umboni kuti akukondwela naye.” Kodi Mulungu anacita bwanji zimenezo? Inoki atatsala pang’ono kufa, mwina Mulungu anamuonetsa masomphenya a dziko lapansi la paradaiso. Inoki anagona mu imfa ali na umboni umenewu wakuti Yehova akukondwela naye. Polemba za Inoki komanso amuna ndi akazi ena okhulupilika, mtumwi Paulo anati: “Onsewa anafa ali ndi cikhulupililo.” (Aheberi 11:13) N’kutheka kuti pambuyo pake, adani a Inoki anafuna-funa mtembo wake, koma ‘sanaupeze kwina kulikonse.’ Mwina Yehova anabisa mtembo wa Inoki n’colinga cakuti anthu asauseŵenzetse pocilikiza kulambila konama, kapena kuugwilitsila nchito m’njila zina zolakwika.b

Mogwilizana ndi mfundo za m’Malemba zimenezi, tiyeni tiyelekezele kuti tikuona mmene moyo wa Inoki unathela. Koma tikumbukile kuti zimenezi n’zongoyelekezela cabe. Iye anali kuthawa ndipo analema ngako. Adani ake anali kumupitikitsa ali wokwiya kwambili cifukwa ca uthenga wake wa ciweluzo. Ndiyeno, Inoki anapeza malo obisalapo ndipo anapumula kwa kanthawi, koma anadziŵa kuti adaniwo amupezabe. Anadziŵanso kuti watsala pang’ono kuphedwa mwankhanza. Conco, pamene anali kupumula anapemphela kwa Mulungu wake. Atapemphela, mtima wake unakhala pansi. Ndiyeno, Inoki anaona masomphenya ocititsa cidwi. Zimene anaona zinali kuoneka monga zeni-zeni cakuti anaiwalilatu mavuto onse amene anali kukumana nawo.

Inoki wabisala m’phanga ndipo adani ake apitilila

Inoki ayenela kuti anali pafupi kuphedwa mwankhanza na adani ake pamene Yehova anamusamutsa

N’kutheka kuti m’masomphenyawo, iye anaona dziko losiyana kwambili na limene anali kukhalamo. Dzikolo linali lokongola monga munda wa Edeni. Koma munalibe akerubi oletsa anthu kuloŵamo. M’dzikolo munali amuna ndi akazi ambili, ndipo onse anali athanzi ndi amphamvu. Iwo anali kukhala mwamtendele. Munalibe cidani kapena anthu ozunza anzawo cifukwa ca cipembedzo, zinthu zimene zinali zofala m’nthawi ya Inoki. Ataona zimenezi, Inoki anazindikila kuti Yehova amam’konda ndi kukondwela naye. Iye anadziŵa kuti dziko limenelo ndiwo malo abwino amene anafunika kukhalamo, ndiponso kuti mtsogolo kudzakhala kwawo kweni-kweni. Pamene mtendele wa m’maganizo mwake unali kuwonjezeleka, Inoki anagona tulo twa imfa.

Inoki ni wakufa mpaka lelo, koma Yehova, Mulungu amene amakwanitsa kukumbukila ciliconse, akali kumukumbukilabe. Monga mmene Yesu analonjezela, tsiku lidzafika pamene onse amene Mulungu akuwakumbukila adzamva mau a Khiristu, ndipo adzauka ndi kukhala m’dziko lokongola ndi lamtendele.—Yohane 5:28, 29.

Kodi mungakonde kudzakhala m’dziko laconco? Zidzakhala zokondweletsa kwambili kuonana ndi Inoki. Ganizilani zinthu zokondweletsa zimene tidzamva kwa iye. Mwina Inoki adzatiuza ngati zimene tiganiza zokhudza imfa yake n’zoona. Komabe, pali pano tingaphunzile cinthu cina cofunika ngako pa citsanzo cake. Pambuyo pokamba za Inoki, Paulo anati: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Cimeneci ni cifukwa cabwino kwambili cotilimbikitsa kukhala olimba mtima ndi acikhulupililo ngati Inoki.

a Akatswili ena a Baibo amakamba kuti Yuda anagwila mau buku lina-lake lochedwa Buku la Inoki. Koma buku limeneli ndi lokayikitsa ndipo amene analemba sadziŵika, ngakhale kuti ena amanama kuti linalembedwa ndi Inoki. M’buku limeneli muli ulosi wazoona wa Inoki, koma cioneka kuti mau a ulosi amenewa anatengedwa ku zolemba zakale zimene masiku ano kulibe, kapena ku nkhani zimene anthu anali kukamba. Mwina Yuda nayenso anatenga ulosi wa Inoki kucokela ku magwelo akale amenewa. N’kuthekanso kuti Yuda anaphunzila za Inoki kucokela kwa Yesu. Yesu anali kuona zocita za Inoki cifukwa cakuti pamene Inoki anali na moyo pa dziko lapansi, Yesuyo anali kumwamba.

b N’zimenenso Mulungu anacita ndi mtembo wa Mose ndi wa Yesu. Iye anaonetsetsa kuti mitembo yawo ndi yotetezeka n’colinga cakuti anthu asaiseŵenzetse molakwika.—Deuteronomo 34:5, 6; Luka 24:3-6; Yuda 9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani