Kodi Mudziŵa?
Kodi Ayuda anali na cizoloŵezi canji cimene cinapangitsa Yesu kuwaletsa kulumbila?
M’CILAMULO CA MOSE, kulumbila nthawi zina kunali koyenelela. Komabe, anthu ambili m’nthawi ya Yesu anali kulumbila mwacisawawa. Iwo anali kucita zimenezo n’colinga cakuti anthu ena akhulupilile zokamba zawo. Koma kaŵili konse, Yesu anawadzudzula cifukwa ca khalidwe lawolo. Mmalomwake, anawauza kuti: “Tangotsimikizani kuti mukati ‘Inde’ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayi’ akhaledi ayi.”—Mat. 5:33-37; 23:16-22.
Malinga n’zimene dikishonale ina inakamba, umboni wakuti “Ayuda anali kukonda kulumbila pa zilizonse,” ni wakuti m’buku laciyuda lochedwa Talmud muli malangizo ambili ofotokoza malumbilo amene anali ololeka kuwasintha ndi amene sanali ololeka kuwasintha.—Theological Dictionary of the New Testament.
Sikuti ni Yesu cabe amene anadzudzula Ayuda cifukwa ca khalidwe limeneli. Nayenso katswili wa mbili yakale ya Ayuda, dzina lake Flavius Josephus anakambako za kagulu kena ka Ayuda. Iye anati: “Iwo amapewa kulumbila cifukwa amaona kuti n’koipa kwambili kuposa kunama. Iwo amakhulupilila kuti ngati munthu amacita kulumbila kuti anthu am’khulupilile, ndiye kuti ni wabodza.” Komanso, buku lina laciyuda lochedwa Wisdom of Sirach, kapena kuti Ecclesiasticus, (23:11) linati: “Munthu amene amakonda kulumbila ni woipa kwambili.” Yesu anawadzudzula Ayuda cifukwa cotenga malumbilo mopepuka. Conco, ngati nthawi zonse timakamba zoona, sitingafunike kucita kulumbila kuti anthu atikhulupilile.