Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndani?
Mulungu anauza olemba Baibo angapo ndithu kulemba zimene zinali kudzathandiza anthu kudziŵa amene adzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Wolamulila ameneyu
Adzasankhidwa na Mulungu. “Inetu ndakhazika mfumu yanga . . . Ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala colowa cako, ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.”—Salimo 2:6, 8.
Adzaloŵa ufumu wa Mfumu Davide. “Kwabadwa mwana. Ife tapatsidwa mwana wamwamuna . . . Ulamulilo wake wangati wa kalonga udzafika kutali ndipo mtendele sudzatha pampando wacifumu wa Davide ndiponso mu ufumu wake, kuti iye acititse ufumuwo kukhazikika.”—Yesaya 9:6, 7.
Adzabadwila ku Betelehemu. “Iwe Betelehemu . . . , mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulila . . . Iye adzakhala wamkulu mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Mika 5:2, 4.
Anthu adzam’kana ndipo adzamupha. “Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake. . . . Iye anabayidwa cifukwa ca zolakwa zathu.”—Yesaya 53:3, 5.
Adzaukitsidwa kwa akufa na kupatsidwa ulemelelo. “Simudzasiya moyo wanga m’Manda. Simudzalola kuti wokhulupilika wanu aone dzenje. . . . kKudzanja lanu lamanja kuli cimwemwe mpaka muyaya.”—Salimo 16:10, 11.
Cifukwa Cake Yesu Khristu Adzakhala Wolamulila Wabwino Kwambili
M’mbili yonse ya anthu, zinthu zonsezi zinakwanilitsidwa ndendende pa munthu mmodzi, amene ndiye Wolamulila woyenelela. Ndipo munthuyo ni Yesu Khristu. Mngelo anacita kuuza Mariya mayi wake wa Yesu kuti: “Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu wa Davide atate wake, . . . moti Ufumu wake sudzatha konse.”—Luka 1: 31-33.
Yesu sanakhale wolamulila padziko lapansi. M’malo mwake, iye adzalamulila anthu kucokela kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kodi n’ciani cikum’pangitsa kukhala Wolamulila woyenelela? Tiyeni tione zimene Yesu anacita ali padziko lapansi.
Yesu anali kusamala za anthu. Yesu anali kuthandiza amuna ndi akazi, acicepele komanso okalamba, mosasamala kanthu za kumene anakulila, kapena mapezedwe awo. (Mateyu 9:36; Maliko 10:16) Pamene munthu wakhate anam’condelela kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeletsa,” Yesu anagwidwa cifundo ndipo anam’cilitsa.—Maliko 1:40-42.
Yesu anatiphunzitsa mmene tingakondweletsele Mulungu. Iye anati: “Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” Anakambanso kuti tifunika kucitila ena zinthu zimene ife tingafune kuti iwo aticitile, limene ni khalidwe lopambana. Kuwonjezela apo, anaonetsa kuti Mulungu amacita cidwi osati cabe pa zimene timacita, koma ngakhale pa zimene timaganiza komanso mmene timamvelela. Conco, kuti tikondweletse Mulungu tifunika kulamulila mmene timamvelela mu mtima mwathu. (Mateyu 5:28; 6:24; 7:12) Ndipo kuti tikhale na cimwemwe ceni-ceni, Yesu anagogomeza kuti tifunika kudziŵa zimene Mulungu amafuna kuti tizicita na kucitadi zimenezo.—Luka 11:28.
Yesu anaphunzitsa zimene kukonda ena kumatanthauza. Mawu komanso zocita za Yesu zinali na mphamvu, ndipo zinakhudza mitima ya omumvetsela. Baibo imati: “Khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamulilo.” (Mateyu 7:28, 29) Iye anaŵaphunzitsa kuti: ‘Kondani adani anu.’ Iye anapemphelela ngakhale ena mwa anthu amene anamupha. Iye anati: “Atate, akhululukileni, cifukwa sakudziŵa cimene akucita.”—Mateyu 5:44; Luka 23:34.
Yesu ndiye woyenelela kwambili kukhala Wolamulila wa dziko lonse, amene ni wokoma mtima komanso wothandiza anthu. Koma kodi adzayamba liti kulamulila?