LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 tsa. 13
  • Madalitso kwa Amene Amathandiza Ofunikila Thandizo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Madalitso kwa Amene Amathandiza Ofunikila Thandizo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA
  • ZIMENE KUTHANDIZA WOFUNIKILA THANDIZO KUMATANTHAUZA
  • Fanizo la Msamariya Wacifundo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 tsa. 13
Akuseŵenzetsa mapu kuonetsa munthu wina mmene angayendele kuti afike kumene akupita.

Kodi mungathandizeko ena mosasamala kanthu za msinkhu, dziko, kapena cipembedzo cawo?

Madalitso kwa Amene Amathandiza Ofunikila Thandizo

Zungulile dziko lapansi, anthu ambili alibe cakudya na nyumba. Ena amafuna cabe kukhala na ciyembekezo ca zakutsogolo. Kodi kuthandiza anthu otelo kungatipangitse bwanji kukhala oyanjidwa na Mulungu, komanso kulandila madalitso ake?

ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA

“Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.”—MIYAMBO 19:17.

ZIMENE KUTHANDIZA WOFUNIKILA THANDIZO KUMATANTHAUZA

Yesu anafotokoza fanizo lokhudza munthu wina amene anavulazidwa ndi acifwamba na kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Luka 10:29-37) Koma munthu wina wacilendo anaimilila, na kusamalila munthuyo amene anavulazidwa kwambili. Iye anacita zimenezi ngakhale kuti anali osiyana mtundu na munthuyo.

Munthu wokoma mtima ameneyo anapeleka cithandizo coyambilila ca cipatala kwa munthu wovulazidwayo, na kum’thandiza pa zofunikila zake kuthupi, komanso kum’tonthoza pavuto lake.

Kodi tiphunzilapo ciani pa fanizoli? Yesu anaonetsa kuti tiyenela kuyesetsa kuthandiza ofunikila thandizo mulimonse mmene tingathele. (Miyambo 14:31) Malemba Oyela amaphunzitsa kuti posacedwa, Mulungu adzacotsapo umphawi na mavuto. Koma mwina tingadzifunse kuti, kodi Mulungu adzawacotsapo motani mavuto komanso liti? Nkhani yotsatila idzafotokoza madalitso amene Mlengi wathu wacikondi watisungila.

“MULUNGU SANANISIYE NEKHA”!

Yosimbidwa na munthu wocokela ku Gambia

“N’tafika ku Europe n’nalibe ciliconse. Sin’nali kuseŵenza, n’nalibe ndalama, komanso nyumba. Ziphunzitso za m’Malemba Oyela zinanithandiza kupilila mavutowo, kulimbika pa nchito, komanso kuthandiza ena m’malo mongokhalila kupempha–pempha thandizo. Mulungu sananisiye nekha, ndipo napeza madalitso ake!”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani