Mmene Nkhondo Zimatikhudzila Tonsefe
“Kucokela pa Nkhondo Yaciwili ya Padziko Lonse, nkhondo zaculuka kwambili. Ndipo anthu 2 biliyoni, kutanthauza kuti munthu mmodzi pa anthu 4 alionse padziko lapansi, akukhala kumadela komwe kukucitika nkhondo.”
Anatelo Amina J. Mohammed, waciwili kwa Kalembela Wamkulu wa Bungwe la United Nations pa January 26, 2023.
Mwadzidzidzi, nkhondo ingabuke ngakhale kumalo kumene kuli mtendele. Ngakhale anthu amene akukhala kutali ndi kumene kukucitikila nkhondo amakhudzidwa, cifukwa zimene zikucitika m’dziko lina zimakhudzanso maiko ena. Ndipo pambuyo pakuti nkhondo yatha, mavuto obwela cifukwa ca nkhondo amatenga nthawi yaitali kuti athe. Onani zitsanzo izi:
Njala. Bungwe Loona za Cakudya Padziko Lonse linati “nkhondo ndiyo cinthu cacikulu cimene cimabweletsa njala padzikoli. Anthu ambili amene akuvutika ndi njala amakhala m’madela amene mukucitika nkhondo.”
Matenda a maganizo komanso matenda ena. Zikaoneka kuti nkhondo ikhoza kubuka m’dziko linalake, anthu a m’dzikolo amakhala ndi nkhawa yaikulu ndiponso amapanikizika maganizo. Anthu amene akukhala m’madela amene mukucitika nkhondo, amakhala pa ciwopsezo covulazidwa komanso kudwala matenda a maganizo. Ndipo n’zomvetsa cisoni kuti nthawi zambili salandila cithandizo ca mankhwala cimene akufunikila.
Anthu amakakamizika kuthawa kwawo. Malinga ndi bungwe la United Nations Loona za Anthu Othawa Kwawo, pofika mu September 2023, padziko lonse lapansi panali anthu oposa 114 miliyoni othawa kwawo. Nkhondo ndiyo cifukwa cacikulu cimene cabweletsa vuto limeneli.
Mavuto a zacuma. Nthawi zambili, nkhondo imabweletsa mavuto a zacuma. Mwacitsanzo, mitengo ya zinthu imakwela. Anthu angavutike ngati boma layamba kutenga ndalama zimene limagwilitsa nchito pa zacipatala komanso pa zamaphunzilo n’kumazigwilitsa nchito pa nkhondo. Komanso pamawonongeka ndalama zambili kuti akonzenso zinthu zimene zinawonongeka cifukwa ca nkhondo.
Kuwonongeka kwa zacilengedwe. Anthu amavutika ngati zinthu zacilengedwe zimene amadalila zawonongedwa. Mwacitsanzo, nkhondo ingacititse kuti madzi, mpweya, ndi nthaka ziwonongeke, ndipo izi zingabweletse matenda osiyanasiyana. Komanso ngakhale patapita zaka zambili pambuyo pa nkhondo, miyoyo ya anthu imakhalabe pa ciwopsezo cifukwa ca mabomba amene anabisidwa m’nthaka.
Conco n’zoonekelatu kuti nkhondo imawononga zinthu komanso ndalama zambili