Kodi Anthu Angakwanitse Kuthetsa Nkhondo?
Anthu amacita nkhondo pa zifukwa zosiyanasiyana. Anthu ena amamenyana pofuna kuti zinthu zisinthe pa zandale, zacuma, kapena kuti athetse zinthu zopanda cilungamo. Ena amamenyana polimbilana malo komanso zinthu zacilengedwe zamtengo wapatali. Nthawi zambili, nkhondo zimacitika cifukwa cosiyana mitundu kapena zipembedzo. Kodi anthu akhala akucita zotani kuti athetse nkhondo ndi kukhazikitsa mtendele? Kodi zimene akucitazo zingabweletsedi mtendele padziko?
Drazen_/E+ via Getty Images
KUPITITSA PATSOGOLO ZACUMA
Colinga: Kuthandiza anthu kuti akhale ndi umoyo wabwino. Kucita izi kungathandize kuthetsa kapena kucepetsa vuto la kusiyana pa zacuma pakati pa anthu, cifukwa nthawi zina zimenezi n’zomwe zimayambitsa nkhondo.
Colepheletsa: Maboma ayenela kusintha mmene amagwilitsila nchito ndalama zawo. Mwacitsanzo, mu 2022, maboma anagwilitsa nchito madola pafupifupi 34.1 biliyoni pofuna kukhazikitsa mtendele padziko lonse komanso kuusunga. Koma ndalama zimenezi sizinali kukwana ngakhale 1 pelesenti ya ndalama zimene maboma anagwilitsa nchito pa zankhondo m’caka cimeneco.
“Timagwilitsa nchito ndalama zoculuka komanso zinthu zina zambili pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi nkhondo, kuposa zimene timagwilitsa nchito pofuna kupewa nkhondo komanso kukhazikitsa mtendele.”—Anatelo António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations.
Zimene Baibo imakamba: Maboma komanso mabungwe angathe kuthandiza anthu osauka, koma sangakwanitse kuthetselatu umphawi.—Deuteronomo 15:11; Mateyo 26:11.
KUKAMBILANA ZA MTENDELE
Colinga: Kupewa kapena kuthetsa mikangano mwamtendele mwa kukambilana ndi kucita zinthu zimene zingapindulitse mbali zonse.
Colepheletsa: Gulu limodzi kapena angapo amene akulimbana angakane kukambilana, kulolela, kapena kuvomeleza mgwilizano. Ndipo mapangano a mtendele amaphwanyidwa mosavuta.
“Si nthawi zonse pamene zokambilana zofuna kubweletsa mtendele zimathandiza. Nthawi zina mgwilizano wa mtendele pakati pa magulu awili olimbana ungakhale ndi zopanda cilungamo zambili, zimene zingacititse kuti m’kupita kwa nthawi padzabukenso nkhondo.”—Raymond F. Smith, American Diplomacy.
Zimene Baibo imakamba: Anthu ayenela ‘kuyesetsa kukhala mwamtendele ndi ena.’ (Salimo 34:14) Koma anthu ambili masiku ano ndi “osakhulupilika, . . . osafuna kugwilizana ndi ena, . . . aciwembu.” (2 Timoteyo 3:1-4) Makhalidwe ngati amenewa amalepheletsa atsogoleli andale oona mtima kuthetsa mikangano.
KUWONONGA NDI KUCEPETSA ZIDA ZANKHONDO
Colinga: Kucepetsa kapena kuwononga zida zankhondo, makamaka za nyukiliya, za mankhwala a poizoni, ndi za tulombo toyambitsa matenda.
Colepheletsa: Nthawi zambili, maiko amakana kucita zimenezi cifukwa coopa kuti angacepe mphamvu kapena angakhale osatetezeka. Koma ngakhale maiko atawononga zida zonse zankhondo, sangathe kuthetsa zinthu zimene zimapangitsa kuti anthu azicita nkhondo.
“Maiko ambili amene analonjeza kuti adzawononga zida zawo zankhondo pambuyo pa caka ca 1991 sanakwanilitse malonjezo awo. Sanakwanilitsenso malonjezo awo akuti adzapewa zinthu zimene zingayambitse nkhondo ndiponso kuti adzacepetsa mikangano pakati pa maiko, n’colinga cakuti pamapeto pake dziko likhale malo amtendele ndi otetezeka.”—“Securing Our Common Future: An Agenda for Disarmament.”
Zimene Baibo imakamba: Anthu ayenela kusiya zida zawo zankhondo ndi “kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo.” (Yesaya 2:4) Koma kuti nkhondo zithe, anthu ayenela kucita zambili cifukwa maganizo aciwawa amacokela mumtima mwa munthu.—Mateyo 15:19.
KUPANGA MGWILIZANO WA MAIKO
Colinga: Maiko amagwilizana kuti adzathandizana ngati limodzi mwa maikowo laukilidwa ndi adani. Iwo amaganiza kuti adani angaope kuyambitsa nkhondo podziwa kuti akacita zimenezo adzafunika kumenyana ndi asilikali a maiko ambili.
Colepheletsa: Kugwilizana kwa maiko angapo kuti azitetezana dziko lina likaukilidwa sikungabweletse mtendele. Zili conco cifukwa si nthawi zonse pamene maiko amakwanilitsa malonjezo awo. Ndipo nthawi zina sagwilizana za mmene adzathandizilana komanso za nthawi pamene angafunike kutelo.
“Ngakhale kuti mabungwe a League of Nations komanso United Nations. . . anayesetsa kuthandiza maboma kuti apange mgwilizano ndi maboma ena, zimenezi sizinaletse nkhondo kucitika.”—“Encyclopedia Britannica.”
Zimene Baibo imakamba: N’zoona kuti mu umodzi muli mphamvu. (Mlaliki 4:12) Komabe, maboma a anthu komanso mabungwe sangathe kubweletsa mtendele ndi citetezo ceniceni. Malemba amati: “Musamadalile atsogoleli a anthu. Palibe munthu amene angakupulumutseni. Akamwalila, amabwelela kufumbi. Tsiku limenelo, mapulani awo onse amatha.”—Salimo 146:3, 4, Today’s English Version.
Ngakhale kuti maboma ambili akuyesetsa kukhazikitsa mtendele, nkhondo zikupitilizabe kucitika