NKHANI YOPHUNZILA 46
NYIMBO 17 “ Nifuna”
Ganizilani za Yesu, Mkulu Wathu wa Ansembe Wacifundo
“ Mkulu wa ansembe amene tili nayeyu, si mkulu wa ansembe amene sangatimvele cisoni pa zofooka zathu.”—AHEB. 4:15.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tikambilane mmene cifundo komanso kumvela cisoni kumapangitsila Yesu kukhala Mkulu wa Ansembe woyenelela. Tionanso mmene tonsefe timapindulila ndi udindo wake masiku ano.
1-2. (a) N’cifukwa ciani Yehova anatuma Mwana wake kubwela padziko lapansi? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino? (Aheberi 5:7-9)
PAFUPI-FUPI zaka 2,000 zapitazo, Yehova Mulungu anatuma Mwana wake wokondedwa padziko lapansi. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi cinali cakuti adzaombole mtundu wa anthu ku ucimo ndi imfa komanso kuti adzathetse mabvuto amene Satana anayambitsa. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 3:8) Yehova anadziwa kuti mabvuto amene Yesu adzakumane nawo akadzakhala munthu padziko lapansi adzam’konzekeletsa kukhala Mkulu wa Ansembe wacifundo kapena kuti womvela ena cisoni. Yesu anayamba kutumikila pa udindowu mu 29 C.E pambuyo pa ubatizo wake.a
2 M’nkhani ino, tikambilane mmene kukhala munthu padziko lapansi kunathandizila Yesu kukhala woyenelela kutumikila monga Mkulu wa Ansembe wacifundo. Kumvetsetsa zimenezi kutithandiza kuti tizikhala omasuka kupemphela kwa Yehova, ngakhale pamene tikudziona ngati osayenela kutelo cifukwa ca zolakwa zathu.—Welengani Aheberi 5:7-9.
MWANA WA MULUNGU WOKONDEKA ATABWELA PADZIKO LAPANSI
3-4. Kodi zinthu zinasintha motani pa umoyo wa Yesu atabwela padziko lapansi?
3 Ambili mwa ife zinthu zinasinthapo mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, mwina tinafunika kusamuka n’kusiya nyumba imene tinali kukonda komanso acibale ndi mabwenzi athu. Masinthidwe amenewa angakhale obvuta. Koma palibe munthu amene zinthu zinasinthako mu umoyo wake monga mmene zinasinthila pa umoyo wa Yesu. Pamene iye anali kumwamba, anali ndi udindo waukulu kwambili pa ana onse auzimu a Yehova. Yehova anali kum’konda kwambili, ndipo iye anali kusangalala kutumikila kudzanja lamanja la Mulungu. (Sal. 16:11; Miy. 8:30) Komabe, lemba la Afilipi 2:7 limati iye analolela ‘kusiya zonse’ zimene anali nazo kumwamba ndi kudzakhala ndi anthu opanda ungwilofe pano padziko lapansi.
4 Komanso, ganizilani mmene zinthu zinalili kuciyambi kwa umoyo wa Yesu padziko lapansi. Iye anabadwila m’banja losauka. Timadziwa zimenezi cifukwa ca nsembe imene makolo ake anapeleka iye atabadwa. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Cina, Mfumu yoipa Herode itadziwa kuti Yesu wabadwa, inafuna kumupha. Pofuna kum’pulumutsa m’manja mwa Herode, makolo ake anathawila naye ku Iguputo. (Mat. 2:13, 15) Uku kunali kusintha kwakukulu tikaganizila umoyo umene Yesu anali nawo kumwamba!
5. Ndi mabvuto otani amene Yesu anaona ali padziko lapansi? Nanga kuona zimenezo kunam’konzekeletsa bwanji kuti adzakwanilitse udindo wokhala Mkulu wa Ansembe? (Onaninso cithunzi.)
5 Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaona mabvuto amene anthu anali kukumana nawo. Mosakaikila, iye anamva mmene cimawawila ngati munthu amene umakonda wamwalila. N’zoonekelatu kuti cinamuwawa kwambili atate ake, Yosefe, atamwalila. Ndiponso pa utumiki wake, Yesu anali kukumana ndi anthu akhate, osaona, ofa ziwalo, ndi makolo ofeledwa ana ao, ndipo anali kuwamvela cisoni. (Mat. 9:2, 6; 15:30; 20:34; Maliko 1:40, 41; Luka 7:13) N’zoona kuti Yesu ali kumwamba anali kuona mabvuto amene anthu anali kukumana nawo. Koma atakhala munthu pano padziko lapansi, anatha kumvetsa bwino mabvuto amene anthu amakumana nawo. (Yes. 53:4) Zocitika mu umoyo wa Yesu zinam’thandiza kumvetsa mabvuto amene anthufe timakumana nawo ndi mmene timabvutikila. Cinanso, mofanana ndi anthu onse, Yesu nayenso anali kutopa, kupanikizika maganizo, ndi kukhumudwa.
Yesu anali kumvetsa mmene anthu anali kumvela ndiponso mabvuto amene anali kukumana nawo (Onani ndime 5)
YESU AMAMVETSA MABVUTO AMENE TIMAKUMANA NAWO
6. Kodi mau ofanizila a mneneli Yesaya atiphunzitsa ciani za cifundo ca Yesu? (Yesaya 42:3)
6 Pa utumiki wake wonse, Yesu anali kuonetsa cifundo cacikulu kwa anthu ofooka ndi kwa anthu amene anali kuonedwa ngati osanunkha kanthu. Mwa kucita izi, anakwanilitsa ulosi. M’malemba aciheberi, anthu acuma, olimba komanso amene zinthu zikuwayendela bwino, amayelekezeledwa ndi dimba lothililidwa bwino kapena mitengo itali-tali yolimba. (Sal. 92:12; Yes. 61:3; Yer. 31:12) Koma anthu osowa pogwila kapena otsika amayelekezeledwa ndi bango lophwanyika komanso cingwe ca nyale cimene catsala pang’ono kuzima. Zinthu zimenezi anthu anali kuziona kuti n’zopanda nchito. (Welengani Yesaya 42:3; Mat. 12:20) Mouzilidwa, mneneli Yesaya anagwilitsa nchito mau ofanizila amenewa polosela za cikondi ndi cifundo cimene Yesu adzaonetse kwa anthu wamba amene anali kuonedwa ngati osafunika.
7-8. Kodi Yesu anakwanilitsa bwanji ulosi wa Yesaya?
7 Wolemba Uthenga Wabwino Mateyo anaonetsa kuti Yesu anakwanilitsa ulosi wa mneneli Yesaya wakuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo cingwe ca nyale cimene cikufuka utsi sadzacizimitsa.” Zina mwa zozizwitsa zimene Yesu anacita zinathandiza anthu amene anali ngati bango lophwanyika kapena amene anali ngati cingwe ca nyale cimene catsala pang’ono kuzima. Pa anthu amenewa panali mwamuna wina amene anali ndi khate thupi lonse. Cifukwa ca khatelo, sanali kukhala pakati pa anthu. Iye analibiletu ciyembekezo cakuti angacile kapena kukhalanso ndi mwai wokhala limodzi ndi mabwenzi komanso a m’banja lake. (Luka 5:12, 13) Panalinso mwamuna wina amene anali ndi bvuto losamva, ndipo anali kubvutika kulankhula. Ganizilani mmene iye anali kumvela akaona anthu akulankhulana koma iye osamva zimene akukambilana. (Maliko 7:32, 33) Koma si zokhazi.
8 M’masiku a Yesu, Ayuda ambili anali kukhulupilila kuti anthu amene anali olumala kapena odwala anali kubvutika cifukwa ca macimo ao kapena a makolo ao. (Yoh. 9:2) Cifukwa ca cikhulupililo cabodza cimeneci, anthu amene anali kudwala kapena olumala anali kudziona ngati osafunika. Pokwanilitsa ulosi wa Yesaya, Yesu anawacilitsa anthu amenewo ndi kuwathandiza kudziwa kuti Mulungu amawakonda. Kodi zimenezi zitilimbikitsa bwanji masiku ano?
9. Kodi Aheberi 4:15, 16 ionetsa bwanji kuti mkulu wathu wa ansembe amene ali kumwamba amamveladi cifundo anthu opanda ungwilo?
9 Welengani Aheberi 4:15, 16. Tingakhale otsimikiza kuti Yesu azitimvela cisoni nthawi zonse. Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Munthu amene amamvela ena cisoni amadziwa ndi kumvetsa mmene ena akumvela akakumana ndi mabvuto. Mau acigiriki amene anawamasulila kuti “kumvela ena cisoni” amatanthauza kumva mmene wina akumvela. (Onaninso Aheberi 10:34.) Tikamawelenga nkhani zofotokoza zozizwitsa za Yesu, timaona mmene cifundo cacikulu cinamulimbikitsila kuthandiza anthu ena. Iye sanacilitse anthu cabe cifukwa coti anafunika kutelo. Koma anali kuwakondadi, ndipo anali kufuna kuwathandiza. Mwacitsanzo, pamene Yesu anafuna kucilitsa wakhate, akanatha kucita zimenezi ngakhale ali kutali. M’malomwake, anafika pafupi ndi kum’gwila munthuyo. N’kutheka kuti panali patadutsa zaka kucokela pamene munthu wakhateyo anagwilidwapo! Ndipo pamene anali kucilitsa munthu amene anali ndi bvuto losamva, anam’tengela pambali capatali ndi gulu la anthulo. Ganizilaninso zimene zinacitika pamene mai wina amene anali kucita zoipa analapa n’kusiya kucita zoipa. Maiyo ananyowetsa mapazi a Yesu ndi misozi ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. Mfarisi wina ataona zimenezi, anam’kalipila maiyo, koma mokoma mtima Yesu anam’teteza. (Mat. 8:3; Maliko 7:33; Luka 7:44) Yesu sanapewe anthu odwala kapena amene anali atacita macimo aakulu. Koma anali kuwalola kubwela kwa iye ndipo anali kuwaonetsa cifundo. Nafenso tingakhale otsimikiza kuti iye amatimvela cifundo.
KUTENGELA CITSANZO CA MKULU WATHU WA ANSEMBE
10. Ndi zinthu ziti zimene tingagwilitse nchito masiku ano pothandiza akhungu komanso amene ali ndi bvuto losamva? (Onaninso zithunzi.)
10 Monga otsatila a Yesu okhulupilika, timayesetsa kutengela citsanzo cake mwa kuonetsa cikondi ndi cifundo kwa ena. (1 Pet. 2:21; 3:8) Ngakhale kuti sitingacilitse akhungu kapena osamva, pali zimene tingacite kuti tiwathandize mwauzimu. Mwacitsanzo, mabuku ofotokoza Baibo akupezeka m’zinenelo zamanja zoposa 100. Ndipo pofuna kuthandiza akhungu komanso amene amaona mobvutikila, zofalitsa za anthu osaona zikupezeka m’zinenelo zoposa 60. Ndipo mavidiyo okhala ndi mau ofotokozela amatulutsidwa m’zinenelo zoposa 100. Makonzedwe amenewa athandiza amene ali ndi bvuto losamva komanso akhungu kuyandikila Yehova ndi Mwana wake.
Zofalitsa zathu zofotokoza Baibo zikupezeka m’zinenelo zoposa 1,000
Kumanzele: Zinenelo zamanja zoposa 100
Kulamanja: Zinenelo zoposa 60 za anthu akhungu
(Onani ndime 10)
11. Kodi gulu la Yehova limaonetsa bwanji kuti limaganizila anthu a mitundu yonse ngati mmene Yesu amacitila? (Machitidwe 2:5-7, 33) (Onaninso zithunzi.)
11 Gulu la Yehova likuyesetsa kuthandiza anthu osiyana-siyana kuti ayandikile Yehova. Kumbukilani kuti Yesu ataukitsidwa, anatsanulila mzimu woyela pa ophunzila ake, n’colinga coti onse amene anasonkhana pa cikondwelelo ca Pentekosite athe kumva uthenga wabwino “aliyense m’cinenelo cake.” (Welengani Machitidwe 2:5-7, 33.) Motsogoleledwa ndi iye, gulu la Mulungu limafalitsa mabuku ofotokoza Baibo m’zinenelo zoposa 1,000 kuphatikizapo zinenelo zimene zimalankhulidwa ndi anthu ocepa. Mwacitsanzo, zinenelo zina za ku North America ndi South America zimalankhulidwa ndi anthu ocepa. Komabe, zofalitsa zathu zimamasulidwa ndi kufalitsidwa m’zinenelo zoposa 160 za kumeneko n’colinga coti anthu ambili akhale ndi mwai womvetsela uthenga wabwino. Zofalitsa zathu zimapezekanso m’zilankhulo zoposa 20 za anthu a mtundu wa Roma. Ndipo anthu ambili amene amalankhula zinenelozi aphunzila coonadi.
Kumanzele: Zinenelo zoposa 160 za Amerindian
Kulamanja: Zinenelo zoposa 20 za anthu a mtundu wa Roma
(Onani ndime 11)
12. Kodi gulu la Yehova limawathandizanso bwanji anthu masiku ano?
12 Kuonjezela pa kuyang’anila nchito yolalikila, gulu la Yehova limapelekanso thandizo kwa anthu amene akumana ndi tsoka la zacilengedwe. Kuti zimenezi zitheke, abale ndi alongo masauzande amadzipeleka kuti athandize abale ndi alongo ao amene akufunikila thandizo. Kuonjezela apo, gulu la Mulungu limamanganso malo olambilila kumene anthu amasonkhana kuti aphunzile za cikondi ca Mulungu pa iwo.
MKULU WATHU WA ANSEMBE ANGAKUTHANDIZENI
13. Kodi Yesu amatithandiza m’njila zina ziti?
13 Pokhala m’busa wabwino, Yesu amaonetsetsa kuti aliyense wa ife akusamalidwa bwino mwauzimu. (Yoh. 10:14; Aef. 4:7) Nthawi zina, tingalefuke kwambili n’kumadziona ngati cingwe ca nyale cimene catsala pang’ono kuzima kapena bango lophwanyika. Izi zingacitike cifukwa ca kudwala kwambili, zophophonya zathu, kapena cifukwa cakuti Mkhristu mnzathu anatikhumudwitsa. Zikakhala telo, tingayambe kuganizila kwambili za mabvuto athu ndi kuiwala za ciyembekezo cathu. Koma kumbukilani kuti Yesu amaona zimene mukupitamo, ndipo amamvetsa mmene mukumvela. Cifundo cimene Yesu ali naco cimamusonkhezela kuti akuthandizeni. Mwacitsanzo, pogwilitsa nchito mzimu woyela, iye angakupatseni mphamvu mukafooka. (Yoh. 16:7; Tito 3:6) Kuwonjezela apo, angasewenzetse “mphatso za amuna” kapena abale ndi alongo ena kuti akulimbikitseni ndi kukuthandizani.—Aef. 4:8.
14. Tingatani tikalefuka?
14 Mukalefuka, muziganizila za udindo wa Yesu monga mkulu wathu wa ansembe. Kumbukilani kuti Yehova anam’tuma padziko lapansi osati cabe kuti adzapeleke moyo wake monga dipo, koma kuti amuthandizenso kumvetsa mabvuto amene anthu opanda ungwilofe timakumana nawo. Tikalefuka cifukwa ca macimo kapena zophophonya zathu, Yesu ndi wokonzeka kutithandiza “pa nthawi yoyenela.”—Aheb. 4:15, 16.
15. Fotokozani citsanzo coonetsa zimene zinathandiza munthu wina kubwelela mumpingo.
15 Yesu akutsogolelanso anthu ake pa nchito yofuna-funa ndi kuthandiza anthu amene anasocela kuti abwelelenso kwa Yehova. (Mat.18:12, 13) Ganizilani zimene zinacitikila munthu wina, dzina lake Stefano.b Pambuyo pokhala wocotsedwa kwa zaka 12, anaganiza zopita kumisonkhano. Iye anati: “Zinali zobvuta kwa ine. Komabe n’nali kufuna kubwelela kwa Yehova. Akulu amene ndinaonana nawo anandipangitsa kukhala womasuka. Nthawi zina maganizo odziona ngati wacabe-cabe anali kundibwelela moti n’nali kufooka. Akulu anandikumbutsa kuti Yehova ndi Yesu akufuna kuti ndisamadzione ngati wolephela. Nditabwezeletsedwa, abale ndi alongo anationetsa cikondi. Kenako, mkazi wanga anayamba kuphunzila Baibo ndipo pano tikutumikila Yehova pamodzi.” N’zosacita kufunsa kuti mkulu wathu wa ansembe amasangalala akaona anthu amene alapa akuthandizidwa kubwelela mumpingo!
16. N’cifukwa ciani ndinu woyamikila kukhala ndi Mkulu wa Ansembe wacifundo?
16 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anapeleka thandizo la panthawi yake kwa anthu osiyana-siyana. Masiku anonso, tingakhale ndi cikhulupililo cakuti adzatithandiza tikafunikila thandizo. Ndipo m’dziko latsopano adzathandiza anthu omvela kumasuka kothelatu ku mabvuto obwela cifukwa ca ucimo ndi kupanda ungwilo. Ndife oyamikila cotani nanga kwa Mulungu wathu Yehova amene, mosonkhezeledwa ndi cikondi cake cacikulu komanso cifundo, anaika Mwana wake kukhala mkulu wathu wa ansembe wacifundo!
Nyimbo 13 Khristu ni Citsanzo Cathu
a Kuti mudziwe zambili za mmene udindo wa Yesu unalowela m’malo mwa udindo wa Mkulu wa Ansembe waciyuda, onani nkhani yakuti “Yamikilani Mwayi Wanu Wolambila Yehova M’kacisi Wake Wauzimu” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2023, tsamba 26, ndime 7-9.
b Maina ena asinthidwa.