-
Deuteronomo 6:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mʼtsogolo mwana wanu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani zimatanthauza chiyani?’ 21 mwana wanuyo mudzamuyankhe kuti, ‘Tinali akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu. 22 Choncho Yehova anapitiriza kuchita zizindikiro ndi zodabwitsa zazikulu ndiponso zowononga mu Iguputo monse,+ kwa Farao ndi kwa anthu onse amʼnyumba mwake, ife tikuona.+
-