-
Levitiko 8:18-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kenako anatenga nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza ndipo Aroni ndi ana ake anaika manja awo pamutu pa nkhosayo.+ 19 Ndiyeno Mose anapha nkhosayo nʼkuwaza magazi ake mbali zonse za guwa lansembe. 20 Anaduladula nkhosayo ndipo Mose anatenga mutu wake, nyama yoduladulayo ndi mafuta ake,* nʼkuziwotcha. 21 Anatsuka matumbo ndi ziboda ndipo Mose anawotcha paguwa lansembe nkhosa yonseyo. Inali nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa.* Komanso inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
-
-
Levitiko 9:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza ndipo ana ake anamupatsa magazi a nyamayo. Atatero iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 13 Kenako anamʼpatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu ndipo anaziwotcha paguwa lansembe. 14 Atatero anatsuka matumbo komanso ziboda, nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza.
-