-
Numeri 15:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakafika mʼdziko limene ndikukupatsani kuti muzikakhalamo,+ 3 ndipo mukamakapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, kaya ndi ya ngʼombe kapena ya nkhosa, kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapena nsembe yaufulu, kapenanso nsembe imene mukupereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti ikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova,+ 4 munthu amene akupereka nsembeyo, azikaperekanso kwa Yehova nsembe yambewu ya ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*
-