-
Levitiko 4:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako azichotsa mafuta onse a ngʼombe ya nsembe yamachimo, kuphatikizapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse apamatumbo. 9 Azichotsanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 10 Zinthu zimenezi zizikhala zofanana ndi zomwe azichotsa pa ngʼombe ya nsembe yamgwirizano.+ Ndipo wansembe aziziwotcha paguwa lansembe zopsereza.
-