-
Numeri 5:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ndiyeno wansembeyo azitenga nsembe yambewu yansanje+ imene ili mʼmanja mwa mkaziyo, nʼkuiyendetsa uku ndi uku pamaso pa Yehova. Akatero, aziibweretsa pafupi ndi guwa lansembe. 26 Wansembeyo azitapako nsembe yambewuyo kuimira nsembe yonseyo, nʼkuiwotcha paguwa lansembe.+ Pambuyo pake, azipatsa mkaziyo madziwo kuti amwe.
-