-
Levitiko 8:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Atatero anatenga mafuta a nkhosayo, mchira wa mafuta, mafuta onse okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake ndi mwendo wakumbuyo wakumanja.+ 26 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati,+ mtanda umodzi wa mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta+ ndi kamtanda kamodzi ka mkate kopyapyala. Anaziika pamwamba pa mafuta ndi mwendo wakumbuyo wakumanja. 27 Atatero anaika zonsezi mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake nʼkuyamba kuziyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova.
-
-
Levitiko 9:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Koma Aroni anayendetsa uku ndi uku zidalezo ndi mwendo wakumbuyo wakumanja pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Mose analamula.+
-