-
Levitiko 8:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kenako Mose anazitenga mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza. Zinthu zimenezi zinali nsembe yowaikira kuti akhale ansembe, yakafungo kosangalatsa.* Inali nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-
-
Numeri 6:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tsopano lamulo lokhudza Mnaziri ndi ili: Pa tsiku limene masiku a unaziri+ wake atha, azimubweretsa pakhomo la chihema chokumanako.
-
-
Numeri 6:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Wansembe azitenga mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Azitenganso mʼdengumo mkate woboola pakati wopanda zofufumitsa ndi kamkate kopyapyala kopanda zofufumitsa. Zinthuzi aziike mʼmanja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake.
-