17 Mwamuna akagona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Choncho onse awiri aziphedwa pamaso pa anthu a mtundu wawo. Iye wachititsa manyazi mchemwali wake ndipo aziyankha mlandu wa kulakwa kwakeko.