-
Levitiko 27:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Koma ngati akupereka nyama yodetsedwa+ imene sikuyenera kuperekedwa nsembe kwa Yehova, azikaonetsa nyamayo kwa wansembe. 12 Wansembe azinena mtengo wake mogwirizana ndi mmene nyamayo ilili, kaya ndi yabwino kapena yoipa. Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 13 Koma ngati akufuna kuiwombola, azipereka mtengo wa nyamayo womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.+
-