-
Numeri 19:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Munthu amene si wodetsedwa uja awaze munthu wodetsedwayo madziwo pa tsiku lachitatu komanso pa tsiku la 7.+ Ndipo pa tsiku la 7 lomwelo amuyeretse ku tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake nʼkusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyera.
20 Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, aziphedwa kuti asakhalenso mumpingowo,+ chifukwa wadetsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera, choncho ndi wodetsedwa.
-