-
Yoswa 1:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno Yoswa anauza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti: 13 “Kumbukirani mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani+ akuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndipo wakupatsani dziko ili. 14 Akazi anu ndi ana anu atsale limodzi ndi ziweto zanu kutsidya lino la Yorodano,+ pamalo amene Mose wakupatsani. Koma asilikali amphamvu nonsenu,+ muwoloke ndipo muzikayenda patsogolo pa abale anu,+ mutakonzeka kumenya nkhondo. Muyenera kuwathandiza.
-