29 Komanso Mose anapereka cholowa kwa hafu ya fuko la Manase motsatira mabanja awo.+ 30 Dera lawo linayambira ku Mahanaimu,+ dera lonse la Basana, dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Mfumu Ogi ya Basana ndiponso midzi yonse yaingʼono ya Yairi+ ku Basana. Dera lawoli linali ndi matauni 60.