-
Deuteronomo 3:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni. 17 Ndinawapatsanso Araba, mtsinje wa Yorodano ndi malo amʼmbali mwa mtsinjewo, kuchokera ku Kinereti* mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere* imene ili mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga, chakumʼmawa.+
-
-
Yoswa 11:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Yabini mfumu ya ku Hazori atangomva zimenezi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni,+ mfumu ya ku Simironi ndi mfumu ya ku Akasafu.+ 2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amʼdera lamapiri kumpoto, mafumu amʼchigwa* chakumʼmwera kwa Kinereti, mafumu a ku Sefela ndiponso mafumu okhala mʼmapiri a Dori+ kumadzulo.
-