-
Levitiko 25:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Koma nyumba za Alevi zimene zili mʼmizinda yawo,+ Aleviwo azikhala ndi ufulu woziwombola mpaka kalekale. 33 Ndipo ngati Mlevi anagulitsa nyumba mumzinda wawo ndipo sanaiwombole, izibwezedwa kwa Mleviyo mʼChaka cha Ufulu.+ Zizikhala choncho chifukwa nyumba zamʼmizinda ya Alevi pakati pa Aisiraeli ndi za Aleviwo basi.+ 34 Komanso, asagulitse malo odyetserako ziweto+ ozungulira mizinda yawo, chifukwa amenewo ndi malo awo mpaka kalekale.
-