13 Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto,
21 Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto mʼdera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto,
27 Ana a Gerisoni+ a mʼmabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase. Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Beesitera ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri.
32 Kuchokera mʼfuko la Nafitali, anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake, wa Kedesi+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse inalipo mizinda itatu.
38 Kuchokera mʼfuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto,