-
Numeri 14:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu kwa zaka 40,+ ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu,* mpaka womalizira kufa wa inu atagona mʼmanda mʼchipululu muno.+ 34 Mudzalangidwa mogwirizana ndi kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, kwa masiku 40.+ Mudzalangidwa kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi, kuti mudziwe kuipa kotsutsana ndi ine.*
-