-
Levitiko 6:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe.
-
-
Numeri 28:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse,* muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ 12 Pa ngʼombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wothira mafuta wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yake yambewu.+ Nkhosa yamphongo imodziyo muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta, wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+
-
-
Numeri 29:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo mogwirizana ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zowotcha pamoto zakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
-