-
Numeri 3:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Upereke Alevi kwa Aroni ndi ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera kwa Aisiraeli.+
-
-
Numeri 8:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Pambuyo pake, Aleviwo azitumikira pachihema chokumanako. Uzichita zimenezi powayeretsa ndi kuwapereka monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku. 16 Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa Aisiraeli. Ine ndikuwatenga kukhala anga mʼmalo mwa onse oyamba kubadwa* pakati pa Aisiraeli.+
-