19 Ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa Aisiraeli. Aleviwo adzatumikira mʼmalo mwa Aisiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a Aisiraeli kuti mliri usagwe pakati pawo+ chifukwa Aisiraeliwo ayandikira malo oyera.”