-
Levitiko 27:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Koma zinthu zimene munthu wapereka kwa Yehova monga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kuchokera pa katundu wake, sizikuyenera kugulitsidwa kapena kuwomboledwa, kaya ndi munthu, nyama kapena munda. Chinthu chilichonse chimene munthu wapereka kwa Yehova ndi chopatulika koposa.+
-
-
Levitiko 27:30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Chakhumi chilichonse+ cha zinthu zamʼdzikolo, kaya ndi zokolola zamʼmunda kapena zipatso zamʼmitengo, ndi za Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova.
-
-
Numeri 18:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Zinthu izinso zizikhala zako: mphatso zonse za Aisiraeli,+ limodzi ndi nsembe zawo zonse zoyendetsa uku ndi uku+ zimene azipereka. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna komanso ana ako aakazi kuti zikhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.+
-