-
Levitiko 6:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe.
-
-
Levitiko 10:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala kuti: “Tengani nsembe yambewu imene yatsala pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda zofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe,+ chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+ 13 Mudye nsembeyo mʼmalo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi nʼzimene ndalamulidwa.
-