-
Numeri 15:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupititsani, 19 muzikapereka chopereka kwa Yehova pa chakudya chilichonse chamʼdzikolo,+ chimene muzikadya.
-
-
Numeri 18:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Zinthu izinso zizikhala zako: mphatso zonse za Aisiraeli,+ limodzi ndi nsembe zawo zonse zoyendetsa uku ndi uku+ zimene azipereka. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna komanso ana ako aakazi kuti zikhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.+
-
-
Numeri 31:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Pa zinthu zimene zaperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ngʼombe, abulu ndi nkhosa kuti zikhale msonkho woperekedwa kwa Yehova. 29 Zimenezi muzitenge pa hafu imene iwo alandire, ndipo muzipereke kwa wansembe Eleazara monga chopereka kwa Yehova.+
-