-
Yoswa 12:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi wa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti ndi ku Edirei. 5 Ankalamulira kuphiri la Herimoni, ku Saleka ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri ndi Amaakati.+ Ankalamuliranso hafu ya Giliyadi mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni, mfumu ya Hesiboni, ankalamulira.+
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumuwa.+ Kenako Mose mtumiki wa Yehova anapereka maderawa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti akhale awo.+
-