-
Numeri 31:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Amunawo anakamenyana ndi Amidiyani, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense. 8 Anthu amene anaphedwawo akuphatikizapo mafumu 5 a Chimidiyani. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga.
-
-
Yoswa 13:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako Mose anagawira cholowa fuko la Rubeni motsatira mabanja awo.
-
-
Yoswa 13:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 mizinda yonse ya mʼmalo okwera ndiponso dziko lonse la Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ili ku Hesiboni.+ Mfumu imeneyi Mose anaigonjetsa+ limodzi ndi atsogoleri a ku Midiyani, Evi, Rekemu, Zuri, Hura, ndi Reba.+ Amenewa anali mafumu omwe anali pansi pa ulamuliro wa Sihoni ndipo ankakhala mʼdzikolo.
-