-
Numeri 22:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Ndiyeno buluyo ataona mngelo wa Yehova ataima pamsewu lupanga lake lili mʼmanja, anayesa kuchoka mumsewu nʼkupatukira kutchire. Koma Balamu anayamba kumʼkwapula kuti abwerere mumsewu.
-
-
Numeri 22:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anayamba kudzikanikizira kukhoma, moti anakanikiziranso phazi la Balamu kukhomako. Ndipo Balamu anayamba kumʼkwapulanso buluyo.
-
-
Numeri 22:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anangokhala pansi, Balamu ali pamsana pake. Choncho Balamu anapsa mtima koopsa, ndipo anapitiriza kumukwapula ndi ndodo yake.
-