-
Deuteronomo 4:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga pakati panu munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori.+
-
-
Yoswa 22:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kodi zoipa zimene tinachita ku Peori zatichepera? Sitinadziyeretsebe ku tchimo limene lija mpaka lero, ngakhale kuti mliri unagwera anthu a Yehova.+
-
-
Hoseya 9:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zamʼchipululu.+
Ndinaona makolo anu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu.
-