23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Pitani mukatenge dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ inu munapandukiranso lamulo la Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake.