-
Oweruza 21:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Anayamba kufunsana kuti: “Pa mafuko onse a Isiraeli ndi ndani sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?”+ Ndiyeno anaona kuti panalibe aliyense wochokera ku Yabesi-giliyadi amene anabwera kumsasa kumene kunali mpingowo.
-
-
1 Samueli 31:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Anthu a ku Yabesi-giliyadi+ atamva zimene Afilisiti anamuchita Sauli, 12 asilikali onse ananyamuka nʼkuyenda usiku wonse ndipo anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pakhoma la mzinda wa Beti-sani. Kenako anabwerera ku Yabesi nʼkutentha mitemboyo kumeneko.
-