-
1 Mafumu 1:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Ndiyeno wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta+ mutenti+ nʼkudzoza Solomo.+ Zitatero anthuwo anayamba kuliza lipenga nʼkumafuula kuti: “Mfumu Solomo akhale ndi moyo wautali!” 40 Atatero anthuwo anayamba kumulondola ndipo ankaimba zitoliro akusangalala kwambiri, moti nthaka inangʼambika chifukwa cha phokoso lawo.+
-
-
1 Mbiri 12:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Anthuwa anakhala kumeneko ndi Davide masiku atatu ndipo ankadya ndi kumwa zimene abale awo anawakonzera. 40 Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara, Zebuloni ndi Nafitali, ankabweretsa chakudya pa abulu, ngamila, nyulu* ndi ngʼombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa. Anabweretsanso makeke a nkhuyu, makeke a mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe ndi nkhosa. Anabweretsa zambirimbiri chifukwa anthu mu Isiraeli anasangalala kwambiri.
-