12Awa ndi anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga+ pa nthawi imene iye sankayenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa asilikali amphamvu amene anamuthandiza pankhondo.+
20 Davide atapita ku Zikilaga,+ anthu ena a fuko la Manase anapita kumbali yake. Anthuwo anali Adinala, Yozabadi, Yediyaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai. Aliyense anali mtsogoleri wa asilikali 1,000, a fuko la Manase.+