10 Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kwa anthu amumzindawo mfundo za mtendere.+ 11 Ngati anthu amumzindawo akuyankhani mwamtendere nʼkukutsegulirani mageti ake, anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo ndipo azikutumikirani.+