18 Mmodzi wa atumikiwo ananena kuti: “Ine ndinaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu akuimba, ndipo amaimba mwaluso. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso msilikali wamphamvu.+ Ndiwodziwa kulankhula, wooneka bwino+ komanso Yehova ali naye.”+
18 Abisai,+ mchimwene wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu ena atatu. Iye anatenga mkondo wake nʼkupha anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+