-
1 Samueli 29:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Olamulira a Afilisiti ankadutsa ndi magulu awo a asilikali 100 ndi 1,000, ndipo Davide ndi amuna amene ankayenda naye ankabwera pambuyo pawo limodzi ndi Akisi.+ 3 Ndiyeno akalonga a Afilisiti anafunsa kuti: “Kodi Aheberiwa akudzatani kuno?” Akisi anayankha akalonga a Afilisitiwo kuti: “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Mfumu Sauli ya Isiraeli. Iye wakhala ndi ine kwa chaka chimodzi kapena kuposa.+ Kuyambira tsiku limene anathawira kwa ine mpaka lero, sindinamupeze ndi vuto lililonse.” 4 Koma akalonga a Afilisiti anamʼpsera mtima kwambiri Akisi ndipo anati: “Muuzeni abwerere,+ apite kumalo amene munamʼpatsa. Musamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa akhoza kukatitembenukira.+ Mukuganiza kuti munthu ameneyu angachite chiyani kuti mbuye wake amukonde? Akaphatu asilikali athu.
-