-
1 Mbiri 5:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Anthu a hafu ya fuko la Manase+ ankakhala kuyambira ku Basana mpaka ku Baala-herimoni, ku Seniri ndi kuphiri la Herimoni+ ndipo anachuluka kwambiri. 24 Atsogoleri a nyumba za makolo awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahadieli. Onsewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, asilikali amphamvu ndiponso anthu otchuka.
-
-
1 Mbiri 11:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Awa ndi amene anali atsogoleri a asilikali amphamvu a Davide amene anamuthandiza kwambiri kulimbitsa ufumu wake pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu mogwirizana ndi mawu a Yehova okhudza Aisiraeli.+
-