-
Yoswa 13:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya mʼchigwa ya Beti-harana, Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni ndi dera lotsala la dziko la Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndi umene unali malire awo kuchokera kumunsi kwa nyanja ya Kinereti,*+ kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28 Dera limeneli linali cholowa cha anthu a fuko la Gadi chimene anapatsidwa motsatira mabanja awo. Iwo anapatsidwa derali limodzi ndi mizinda komanso midzi ya kumeneko.
-