-
1 Mafumu 7:48-50Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 Solomo anapanga zinthu zonse zapanyumba ya Yehova. Anapanga guwa lansembe+ lagolide komanso tebulo yagolide+ yoikapo mkate wachionetsero. 49 Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino ndipo anaziika pafupi ndi chipinda chamkati, anaika 5 kumanja, 5 kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa agolide,+ nyale zagolide, zopanira zagolide zozimitsira nyale,+ 50 mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa, makapu+ ndiponso zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko za chipinda chamkati,+ kutanthauza Malo Oyera Koposa ndiponso molowa miyendo ya zitseko za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide.
-