34 Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira bambo ake Uziya.+ 35 Komabe sanachotse malo okwezeka ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+ Iye ndi amene anamanga geti lakumtunda la nyumba ya Yehova.+